| Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? | Phunziro 15 |
Kuthandiza Ena Kuchita Chifuniro cha Mulungu |
|
| Kodi n’chifukwa ninji muyenera kuuza ena zimene mukuphunzira? (1) | |
| Kodi ndani amene mungauzeko uthenga wabwino? (2) | |
| Kodi khalidwe lanu lingawakhudze motani ena? (2) | |
| Kodi ndi liti pamene mungalalikire limodzi ndi mpingo? (3) | |
1. Pofika pano, mwaphunzira zinthu zambiri zabwino m’Baibulo. Chidziŵitso chimenechi chiyenera kukusonkhezerani kukulitsa umunthu wachikristu. (Aefeso 4:22-24) Chidziŵitso chimenecho n’chofunika kwambiri kuti mukapeze moyo wosatha. (Yohane 17:3) Komabe, ena afunikanso kumva uthenga wabwino kuti nawonso akapulumuke. Akristu oona onse ayenera kuchitira umboni kwa ena. Ndi lamulo la Mulungu.—Aroma 10:10; 1 Akorinto 9:16; 1 Timoteo 4:16. 2. Mungayambe mwa kuuza aja okhala pafupi nanu zinthu zabwino zimene mukuphunzira. Zisimbeni ku banja lanu, mabwenzi, anzanu akusukulu, ndi akuntchito. Mukhale wokoma mtima ndi woleza mtima pochita zimenezo. (2 Timoteo 2:24, 25) Kumbukirani kuti anthu nthaŵi zambiri amayang’anira kwambiri khalidwe la wina kuposa zonena zake. Chotero khalidwe lanu labwino lingakope ena kuti amvetsere uthenga umene muwauza.—Mateyu 5:16; 1 Petro 3:1, 2, 16. 3. M’kupita kwa nthaŵi, mungayambe kupita kukalalikira limodzi ndi mpingo wakwanuko wa Mboni za Yehova. Njira imeneyi njofunika kwambiri pa kupita kwanu patsogolo. (Mateyu 24:14) Mudzasangalala kwambiri ngati mudzatha kuthandiza wina kukhala mtumiki wa Yehova ndi kupeza moyo wamuyaya!—1 Atesalonika 2:19, 20. |
||
Lofalitsidwa mu 1996 |
|
Copyright © 2006 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. All rights reserved. |
|